Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -




Machitidwe a Atumwi 18:25 - Buku Lopatulika

25 Iyeyo anaphunzitsidwa m'njira ya Ambuye; pokhala nao mzimu wachangu, ananena ndi kuphunzitsa mosamalira zinthu za Yesu, ndiye wodziwa ubatizo wa Yohane wokha;

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

25 Iyeyo anaphunzitsidwa m'njira ya Ambuye; pokhala nao mzimu wachangu, ananena ndi kuphunzitsa mosamalira zinthu za Yesu, ndiye wodziwa ubatizo wa Yohane wokha;

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

25 Iyeyu adaaphunzitsidwa Njira ya Ambuye, ndipo ndi changu chachikulu ankalankhula ndi kuphunzitsa za Yesu molongosoka, chonsecho ankangodziŵa za ubatizo wa Yohane wokha.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

25 Apoloyu anaphunzitsidwa njira ya Ambuye, ndipo anayankhula ndi changu chachikulu naphunzitsa za Yesu molondola, ngakhale amadziwa ubatizo wa Yohane wokha.

Onani mutuwo Koperani




Machitidwe a Atumwi 18:25
27 Mawu Ofanana  

Chifukwa ndamdziwa iye kuti alamulire ana ake ndi banja lake la pambuyo pake, kuti asunge njira ya Yehova, kuchita chilungamo ndi chiweruziro, kuti Yehova akamtengere Abrahamu chomwe anamnenera iye.


Odala angwiro m'mayendedwe ao, akuyenda m'chilamulo cha Yehova.


kuti njira yanu idziwike padziko lapansi, chipulumutso chanu mwa amitundu onse.


Mau a wofuula m'chipululu, Konzani njira ya Yehova, lungamitsani m'dziko loti see khwalala la Mulungu wathu.


Yehova atero, Imani m'njira ndi kuona, funsani za mayendedwe akale, m'menemo muli njira yabwino, muyende m'menemo, ndipo mudzapeza mpumulo wa miyoyo yanu; koma anati, Sitidzayendamo.


Wanzeru ndani, kuti azindikire izi? Waluntha, kuti adziwe izi? Pakuti njira za Yehova zili zoongoka; ndipo olungama adzayendamo, koma olakwa adzagwamo.


Mau a wofuula m'chipululu, konzani khwalala la Ambuye, lungamitsani njira zake.


Ndipo pamene anafika, ananena naye, Mphunzitsi, tidziwa kuti muli woona, ndipo simusamala munthu; pakuti simuyang'ana nkhope ya anthu, koma muphunzitsa njira ya Mulungu moona: Nkuloleka kodi kupereka msonkho kwa Kaisara, kapena iai?


kuti udziwitse zoona zake za mau amene unaphunzira.


Ndipo anthu onse ndi amisonkho omwe, pakumva, anavomereza kuti Mulungu ali wolungama, popeza anabatizidwa iwo ndi ubatizo wa Yohane.


nati, Wodzala ndi chinyengo chonse ndi chenjerero lonse, iwe, mwana wa mdierekezi, mdani wa chilungamo chonse, kodi sudzaleka kuipsa njira zolunjika za Ambuye?


Ameneyo anatsata Paulo ndi ife, nafuula, kuti, Anthu awa ndi akapolo a Mulungu wa Kumwambamwamba, amene akulalikirani inu njira ya chipulumutso.


ndipo iye anayamba kulankhula molimba mtima m'sunagoge, koma pamene anamumva iye Prisila ndi Akwila, anamtenga, namfotokozera njira ya Mulungu mosamalitsa.


Nthawi yomweyo kunali phokoso lambiri kunena za Njirayo.


Ndipo anati, Nanga mwabatizidwa m'chiyani? Ndipo anati, Mu ubatizo wa Yohane.


Koma pamene ena anaumitsa mtima ndi kusamvera, nanenera zoipa Njirayo pamaso pa anthu, anawachokera, napatutsa ophunzira, nafotokozera masiku onse m'sukulu ya Tirano.


napempha kwa iye makalata akunka nao ku Damasiko ku masunagoge, kuti akapeza ena otsata Njirayo, amuna ndi akazi, akawatenge kudza nao omangidwa ku Yerusalemu.


musakhale aulesi m'machitidwe anu; khalani achangu mumzimu, tumikirani Ambuye;


Msilikali sakodwa nazo ntchito wamba, kuti akakondweretse iye amene adamlemba usilikali.


Chifukwa chake muvomerezane wina ndi mnzake machimo anu, ndipo mupempherere wina kwa mnzake kuti muchiritsidwe. Pemphero la munthu wolungama likhoza kwakukulu m'machitidwe ake.


kuti ndiyese nayo Israele ngati adzasunga njira ya Yehova kuyendamo monga anaisunga makolo ao, kapena iai.


Ndipo inenso, kukhale kutali ndi ine, kuchimwira Yehova ndi kuleka kukupemphererani; koma ndidzakulangizani njira yabwino ndi yolungama.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa