Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Luka 1:3 - Buku Lopatulika

3 kuyambira pachiyambi, ndinayesa nkokoma inenso, amene ndinalondalonda mosamalitsa zinthu zonse kuyambira pachiyambi, kulembera kwa iwe tsatanetsatane, Teofilo wabwinotu iwe;

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

3 kuyambira pachiyambi, ndinayesa nkokoma inenso, amene ndinalondalonda mosamalitsa zinthu zonse kuyambira pachiyambi, kulembera kwa iwe tsatanetsatane, Teofilo wabwinotu iwe;

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

3 Tsono popeza kuti inenso ndalondola mosamala kwambiri m'mene zonsezo zidachitikira kuyambira pa chiyambi, ndaganiza kuti nkwabwino kuti ndikulembereni zimenezo mwatsatanetsatane.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

3 Popeza inenso ndafufuza mosamalitsa chilichonse kuyambira pachiyambi, zandikomera kukulemberani mwatsatanetsatane inu wolemekezeka Tiofilo,

Onani mutuwo Koperani




Luka 1:3
17 Mawu Ofanana  

Inu, Yehova, Mulungu wanga, zodabwitsa zanu mudazichita nzambiri, ndipo zolingirira zanu za pa ife; palibe wina wozifotokozera Inu; ndikazisimba ndi kuzitchula, zindichulukira kuziwerenga.


Izi unazichita iwe, ndipo ndinakhala chete Ine; unayesa kuti ndifanana nawe, ndidzakudzudzula, ndi kuchilongosola pamaso pako.


kuti ukadziwitse ntheradi yake ya mau oona, nukabwere ndi mau oona kwa iwo amene anakutumiza?


Ndiponso pokhala wanzeru Mlalikiyo anaphunzitsabe anthu nzeru; inde, anatchera makutu nafunafuna nalongosola miyambi yambiri.


Popeza ambiri anayesa kulongosola nkhani ya zinthu zinachitika pakati pa ife,


Taonani Teofilo inu, mau aja oyamba ndinakonza, za zonse Yesu anayamba kuzichita ndi kuziphunzitsa,


Koma Petro anayamba kuwafotokozera chilongosolere, nanena,


Chifukwa chake ine ndiweruza, kuti tisavute a mwa amitundu amene anatembenukira kwa Mulungu,


chinatikomera ndi mtima umodzi, tisankhe anthu, ndi kuwatumiza kwa inu pamodzi ndi okondedwa anthu Barnabasi ndi Paulo,


Pakuti chinakomera Mzimu Woyera ndi ife, kuti tisasenzetse inu chothodwetsa chachikulu china choposa izi zoyenerazi;


Atakhala kumeneko nthawi, anachoka, napita ku madera osiyanasiyana a dziko la Galatiya ndi la Frijiya, nakhazikitsa ophunzira onse.


Klaudio Lisiasi kwa kazembe womveketsa Felikisi, ndikupatsani moni.


tizilandira ndi chiyamiko chonse, monsemo ndi ponsepo, Felikisi womveka inu.


Koma Paulo anati, Ndilibe misala, Fesito womvekatu; koma nditulutsa mau a choonadi ndi odziletsa.


Koma za Apolo, mbaleyo, ndamuumiriza iye, adze kwa inu pamodzi ndi abale; ndipo sichinali chifuniro chake kuti adze tsopano, koma adzafika pamene aona nthawi.


Koma akhala wokondwera koposa ngati akhala monga momwe ali, monga mwa kuyesa kwanga; ndipo ndinagiza kuti inenso ndili naye Mzimu wa Mulungu.


Ngati ukumbutsa abale zinthu izi, udzakhala mtumiki wabwino wa Khristu Yesu, woleredwa m'mauwo a chikhulupiriro, ndi malangizo abwino amene udawatsata;


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa