Ndipo ine Daniele ndekha ndinaona masomphenyawo; pakuti anthu anali nane sanaone masomphenyawo; koma kunawagwera kunjenjemera kwakukulu, nathawa kubisala.
Luka 1:12 - Buku Lopatulika Ndipo Zekariya anadabwa pamene anamuona, ndipo mantha anamgwira. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Ndipo Zekariya anadabwa pamene anamuona, ndipo mantha anamgwira. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Zakariya adadzidzimuka pomuwona, nachita mantha. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Zakariya ataona mngeloyo, anadzidzimuka ndipo anagwidwa ndi mantha. |
Ndipo ine Daniele ndekha ndinaona masomphenyawo; pakuti anthu anali nane sanaone masomphenyawo; koma kunawagwera kunjenjemera kwakukulu, nathawa kubisala.
Ndipo pamene analowa m'manda, anaona mnyamata alikukhala kumbali ya kudzanja lamanja, wovala mwinjiro woyera; ndipo iwo anadabwa.
Ndipo pompenyetsetsa iye ndi kuopa, anati, Nchiyani, Mbuye? Ndipo anati kwa iye, Mapemphero ako ndi zachifundo zako zinakwera zikhala chikumbutso pamaso pa Mulungu.
Ndipo pamene ndinamuona Iye, ndinagwa pa mapazi ake ngati wakufa; ndipo anaika dzanja lake lamanja pa ine, nati, Usaope, Ine ndine Woyamba ndi Wotsiriza,
Pamenepo Gideoni anaona kuti ndiye mthenga wa Yehova, nati Gideoni, Tsoka ine, Yehova Mulungu! Popeza ndaona mthenga wa Yehova maso ndi maso.