Mulungu ndipo anadalitsa iwo, ndipo adati kwa iwo, Mubalane, muchuluke, mudzaze dziko lapansi, muligonjetse: mulamulire pansomba za m'nyanja, ndi pambalame za m'mlengalenga, ndi pazamoyo zonse zokwawa padziko lapansi.
Genesis 9:7 - Buku Lopatulika Ndi inu, mubalane, muchuluke; muswane padziko lapansi, nimuchuluke m'menemo. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Ndi inu, mubalane, muchuluke; muswane pa dziko lapansi, nimuchuluke m'menemo. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Tsopano mubalane, kuti zidzukulu zanu zidzachulukane ndi kudzabalalika pa dziko lonse lapansi.” Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Inu muberekane ndi kuchulukana kuti mudzaze dziko lonse lapansi ndi kuligonjetsa.” |
Mulungu ndipo anadalitsa iwo, ndipo adati kwa iwo, Mubalane, muchuluke, mudzaze dziko lapansi, muligonjetse: mulamulire pansomba za m'nyanja, ndi pambalame za m'mlengalenga, ndi pazamoyo zonse zokwawa padziko lapansi.
Ndipo Mulungu anati kwa iye, Ine ndine Mulungu Wamphamvuyonse: ubale, uchuluke; mwa iwe mudzatuluka mtundu ndi gulu la mitundu, ndipo mafumu adzatuluka m'chuuno mwako;
Tulutsa pamodzi ndi iwe zamoyo zonse zili ndi iwe za nyama zonse, zouluka, ndi zinyama, ndi zokwawa zonse zakukwawa padziko lapansi; kuti ziswane padziko lapansi, zibalane, zichuluke padziko lapansi.
Ndipo Mulungu anadalitsa Nowa ndi ana ake, nati kwa iwo, Mubalane, muchuluke, mudzaze dziko lapansi.
tengani akazi, balani ana aamuna ndi aakazi; kwatitsani ana anu aamuna, patsani ananu aakazi kwa amuna, kuti abale ana aamuna ndi aakazi; kuti mubalane pamenepo musachepe.