Baibulo la pa intaneti

Zotsatsa


Baibulo lonse Chipangano Chakale Chipangano Chatsopano




Genesis 9:26 - Buku Lopatulika

Ndipo anati, Ayamikike Yehova, Mulungu wa Semu; Kanani akhale kapolo wake.

Onani mutuwo

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

Ndipo anati, Ayamikike Yehova, Mulungu wa Semu; Kanani akhale kapolo wake.

Onani mutuwo

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

“Atamandike Chauta, Mulungu wa Semu, Kanani adzakhale kapolo wa Semuyo.

Onani mutuwo

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

Anatinso, “Atamandike Yehova, Mulungu wa Semu! Kanaani akhale kapolo wa Semu.

Onani mutuwo



Genesis 9:26
15 Mawu Ofanana  

ayamikike Mulungu Wamkulukulu amene wapereka adani ako m'dzanja lako. Ndipo anampatsa iye limodzi la magawo khumi la zonse.


Ndipo anati, Ayamikike Yehova Mulungu wa Ambuyanga Abrahamu amene sanasiye mbuyanga wopanda chifundo chake ndi zoona zake: koma ine Yehova wanditsogolera m'njira ya kunyumba ya abale ake a mbuyanga.


Anthu akutumikire iwe, mitundu ikuweramire iwe; uchite ufumu pa abale ako, ana a amai ako akuweramire iwe. Wotemberereka aliyense akutemberera iwe, wodalitsika aliyense akudalitsa iwe.


Ndipo anayankha Isaki nati kwa Esau, Taona, ndamuyesa iye mkulu wako, ndi abale ake onse ndampatsa iye akhale akapolo ake; ndakhazikitsa iye ndi tirigu ndi vinyo; nanga pamenepo mwana wanga, ndidzakuchitira iwe chiyani?


Udzakhala ndi moyo ndi lupanga lako, nudzakhala kapolo wa mphwako. Ndipo padzakhala pamene udzapulumuka, udzachotsa goli lake pakhosi pako.


ana ao amene adatsala m'dziko, amene ana a Israele sanakhoze kuononga konse, Solomoni anawasenzetsa msonkho wa ntchito kufikira lero.


Odala anthu akuona zotere; odala anthu amene Mulungu wao ndi Yehova.


a iwo ali makolo, ndi kwa iwo anachokera Khristu, monga mwa thupi, ndiye Mulungu wa pamwamba pa zonse wolemekezeka kunthawi zonse. Amen.


Palibe wina ngati Mulungu, Yesuruni iwe, wakuyenda wokwera pathambo, kukuthandiza, ndi pa mitambo mu ukulu wake.


Koma tsopano akhumba lina loposa, ndilo la mu Mwamba; mwa ichi Mulungu sachita manyazi nao poitanidwa Mulungu wao; pakuti adawakonzera mzinda.


Ndipo tsopano mukhale otembereredwa, palibe mmodzi wa inu adzamasuka wosakhala kapolo, ndi kutemera nkhuni, ndi kutungira madzi nyumba ya Mulungu wanga.


Ndipo kunali, atakula mphamvu Israele, anasonkhetsa Akanani, osawaingitsa onse.