Chaka cha mazana asanu ndi limodzi cha moyo wa Nowa, mwezi wachiwiri, tsiku la khumi ndi asanu ndi awiri la mwezi, tsiku lomwelo akasupe onse a madzi aakulu anasefuka, ndi mazenera a kumwamba anatseguka.
Genesis 8:5 - Buku Lopatulika Ndipo madzi analinkuchepa kufikira mwezi wakhumi; mwezi wakhumi tsiku loyamba mwezi ndipo padaoneka mitu ya mapiri. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Ndipo madzi analinkuchepa kufikira mwezi wakhumi; mwezi wakhumi tsiku loyamba mwezi ndipo padaoneka mitu ya mapiri. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Madziwo adanka natsikabe, ndipo pa tsiku loyamba la mwezi wakhumi, nsonga za mapiri zidayamba kuwoneka. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Madzi anapitirira kuphwa mpaka mwezi wa khumi, ndipo pa tsiku loyamba la mwezi wa khumiwo msonga za mapiri zinayamba kuonekera. |
Chaka cha mazana asanu ndi limodzi cha moyo wa Nowa, mwezi wachiwiri, tsiku la khumi ndi asanu ndi awiri la mwezi, tsiku lomwelo akasupe onse a madzi aakulu anasefuka, ndi mazenera a kumwamba anatseguka.
ndipo madzi anaphweraphwerabe padziko lapansi: pamene anatha masiku zana limodzi kudza makumi atatu madzi anachepa.
Ndipo chingalawa chinaima pamapiri a Ararati, mwezi wachisanu ndi chiwiri, tsiku lakhumi ndi asanu ndi awiri la mwezi.
Ndipo panali atapita masiku makumi anai, Nowa anatsegula pa zenera la chingalawa limene analipanga: