Ndipo madzi anapambana, nachuluka ndithu padziko lapansi, ndipo chingalawa chinayandama pamadzi.
Genesis 7:19 - Buku Lopatulika Ndipo madzi anapambana ndithu padziko lapansi; anamizidwa mapiri aatali onse amene anali pansi pathambo lonse. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Ndipo madzi anapambana ndithu pa dziko lapansi; anamizidwa mapiri aatali onse amene anali pansi pa thambo lonse. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Kukwera kwa madzi kudapitirira ndithu mpaka kumiza ndi mapiri aatali omwe. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Madzi a chigumula anabwerabe molimbika motero kuti mapiri ataliatali onse a pa dziko anamizidwa. |
Ndipo madzi anapambana, nachuluka ndithu padziko lapansi, ndipo chingalawa chinayandama pamadzi.
Ndithu akhulupirira mwachabe chithandizo cha kuzitunda, ndi phokoso la kumapiri; ndithu mwa Yehova Mulungu wathu muli chipulumutso cha Israele.