Ndine, taonani, ndipo Ine ndidzadzetsa chigumula cha madzi padziko lapansi, kuti chiononge zamoyo zonse, m'mene muli mpweya wa moyo pansi pathambo; zinthu zonse za m'dziko lapansi zidzafa.
Genesis 7:10 - Buku Lopatulika Ndipo panali pamene anapita masiku asanu ndi awiri, madzi a chigumula anali padziko lapansi. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Ndipo panali pamene anapita masiku asanu ndi awiri, madzi a chigumula anali pa dziko lapansi. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Patangopita masiku asanu ndi aŵiri, chigumula chidafika pa dziko lonse lapansi. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Patapita masiku asanu ndi awiri chigumula chinabwera pa dziko lapansi. |
Ndine, taonani, ndipo Ine ndidzadzetsa chigumula cha madzi padziko lapansi, kuti chiononge zamoyo zonse, m'mene muli mpweya wa moyo pansi pathambo; zinthu zonse za m'dziko lapansi zidzafa.
Pakuti akapita masiku asanu ndi awiri Ine ndidzavumbitsa mvula padziko lapansi masiku makumi anai usana ndi usiku; ndi zinthu zamoyo zonse zomwe ndazipanga ndidzaziononga padziko lapansi.
zinalowa ziwiriziwiri kwa Nowa m'chingalawamo, yamphongo ndi yaikazi, monga momwe Mulungu anamlamulira Nowa.
Anadya, anamwa, anakwatira, anakwatiwa, kufikira tsiku lija Nowa analowa m'chingalawa, ndipo chinadza chigumula, nkuwaononga onsewo.