Ndipo Sara anafa mu Kiriyati-Ariba (ndiwo Hebroni), m'dziko la Kanani; ndipo Abrahamu anadza ku maliro a Sara, kuti amlire.
Genesis 50:1 - Buku Lopatulika Ndipo Yosefe anagwa pa nkhope ya atate wake, namlirira iye nampsompsona iye. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Ndipo Yosefe anagwa pa nkhope ya atate wake, namlirira iye nampsompsona iye. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Pomwepo Yosefe adadzigwetsa pa mtembo wa bambo wake akulira, kwinaku akumpsompsona bambo wake. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Kenaka Yosefe anadzigwetsa pa nkhope ya abambo ake, nawapsompsona kwinaku akulira. |
Ndipo Sara anafa mu Kiriyati-Ariba (ndiwo Hebroni), m'dziko la Kanani; ndipo Abrahamu anadza ku maliro a Sara, kuti amlire.
Ine ndidzatsikira pamodzi ndi iwe ku Ejipito; ndipo Ine ndidzakubwezanso ndithu; ndipo Yosefe adzaika dzanja lake pamaso pako.
Pamene Yakobo anatha kulangiza ana ake aamuna, anafunya mapazi ake pakama, natsirizika, nasonkhanitsidwa kwa anthu a mtundu wake.
Ndipo Yosefe anauza akapolo ake asing'anga kuti akonze atate wake ndi mankhwala osungira thupi: ndipo asing'anga anakonza Israele.
Ndipo Elisa anadwala nthenda ija adafa nayo, namtsikira Yehowasi mfumu ya Israele, namlirira, nati, Atate wanga, atate wanga, galeta wa Israele ndi apakavalo ake!
Ndipo atate inu, musakwiyitse ana anu; komatu muwalere iwo m'maleredwe ndi chilangizo cha Ambuye.
Koma sitifuna, abale, kuti mukhale osadziwa za iwo akugona; kuti mungalire monganso otsalawo, amene alibe chiyembekezo.