Ndipo mudzakhala m'dziko la Goseni, mudzakhala pafupi ndi ine, inu ndi ana anu, ndi ana a ana anu, ndi nkhosa zanu, ndi zoweta zanu, ndi zonse muli nazo;
Genesis 45:9 - Buku Lopatulika Fulumirani. Kwerani kunka kwa atate wanga, muti kwa iye, Chotere ati Yosefe mwana wanu, Mulungu wandiyesa ine mwini Ejipito lonse: tsikirani kwa ine, musachedwe. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Fulumirani. Kwerani kunka kwa atate wanga, muti kwa iye, Chotere ati Yosefe mwana wanu, Mulungu wandiyesa ine mwini Ejipito lonse: tsikirani kwa ine, musachedwe. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Tsopano fulumirani, bwererani kwa bambo wanga, mukamuuze kuti mwana wanu Yosefe akunena kuti, ‘Mulungu wandikuza mpaka kukhala wolamulira Ejipito yense, tsono bwerani kuno, musachedwe. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Tsono fulumirani mubwerere kwa abambo anga ndi kuwawuza kuti, ‘Mwana wanu Yosefe akuti, Mulungu anandisandutsa kukhala mbuye wa dziko lonse la Igupto. Ndiye bwerani kuno musachedwe. |
Ndipo mudzakhala m'dziko la Goseni, mudzakhala pafupi ndi ine, inu ndi ana anu, ndi ana a ana anu, ndi nkhosa zanu, ndi zoweta zanu, ndi zonse muli nazo;
Ndipo mudzafotokozera atate wanga za ulemerero wanga wonse mu Ejipito, ndi zonse mwaziona; ndipo muzifulumira ndi kutsitsira kuno atate wanga.
Ndipo Yosefe anatumiza, naitana Yakobo atate wake, ndi a banja lake lonse, ndiwo anthu makumi asanu ndi awiri mphambu asanu.