Anthu akutumikire iwe, mitundu ikuweramire iwe; uchite ufumu pa abale ako, ana a amai ako akuweramire iwe. Wotemberereka aliyense akutemberera iwe, wodalitsika aliyense akudalitsa iwe.
Genesis 42:10 - Buku Lopatulika Ndipo iwo anati kwa iye, Iai, mbuyanga, koma akapolo anu adzera kudzagula chakudya. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Ndipo iwo anati kwa iye, Iai, mbuyanga, koma akapolo anu adzera kudzagula chakudya. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Iwo aja adayankha kuti, “Iyai mbuyathu, ife atumiki anu tabwera kuti tidzagule chakudya basi. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Iwo anayankha, “Ayi mbuye wathu, antchito anufe tabwera kudzagula chakudya. |
Anthu akutumikire iwe, mitundu ikuweramire iwe; uchite ufumu pa abale ako, ana a amai ako akuweramire iwe. Wotemberereka aliyense akutemberera iwe, wodalitsika aliyense akudalitsa iwe.
Ndipo anayankha Isaki nati kwa Esau, Taona, ndamuyesa iye mkulu wako, ndi abale ake onse ndampatsa iye akhale akapolo ake; ndakhazikitsa iye ndi tirigu ndi vinyo; nanga pamenepo mwana wanga, ndidzakuchitira iwe chiyani?
Abale ake ndipo anati kwa iye, Kodi udzakhala mfumu yathu ndithu? Kapena udzatilamulira ife ndithu kodi? Ndipo anamuda iye koposa chifukwa cha maloto ake ndi mau ake.
Ndipo Obadiya ali m'njira taona, Eliya anakomana naye; iye namdziwa, namgwadira, nati, Ndinu kodi mbuye wanga Eliya?
Ndipo Saulo anazindikira mau ake a Davide, nati, Ndi mau ako awa, mwana wanga Davide? Nati Davide, Ndi mau anga mfumu, mbuye wanga.