Ndipo dzina la wachiwiri anamutcha Efuremu: chifukwa Mulungu anandibalitsa ine m'dziko la kusauka kwanga.
Genesis 41:53 - Buku Lopatulika Ndipo zaka zakuchuluka dzinthu zisanu ndi ziwiri za m'dziko la Ejipito, zinatha. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Ndipo zaka zakuchuluka dzinthu zisanu ndi ziwiri za m'dziko la Ejipito, zinatha. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Zaka zisanu ndi ziŵiri za dzinthu zitatha, Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Zaka zisanu ndi ziwiri za zokolola zochuluka zija zinatha, |
Ndipo dzina la wachiwiri anamutcha Efuremu: chifukwa Mulungu anandibalitsa ine m'dziko la kusauka kwanga.
Ndipo zinayamba kufika zaka zisanu ndi ziwiri za njala, monga ananena Yosefe; ndipo munali njala m'maiko monse; koma m'dziko lonse la Ejipito munali chakudya.
Zaka ziwirizi muli njala m'dziko muno; ndipo zatsala zaka zisanu, zopanda kulima kapena kusenga.
Monga anthu atauka, apepula loto; momwemo, Inu Ambuye, pakuuka mudzapeputsa chithunzithunzi chao.
Koma Abrahamu anati, Mwana, kumbukira kuti unalandira zokoma zako pakukhala m'moyo iwe, momwemonso Lazaro zoipa; ndipo tsopano iye asangalatsidwa pano, koma iwe uzunzidwadi.