Ndipo, taonani, zinatuluka m'mtsinjemo ng'ombe zazikazi zisanu ndi ziwiri za maonekedwe okoma ndi zonenepa; ndipo zinadya mabango.
Genesis 41:4 - Buku Lopatulika Ndipo ng'ombe zazikazi za maonekedwe oipa ndi zoonda zinadya ng'ombe zazikazi zisanu ndi ziwiri za maonekedwe abwino ndi zonenepazo. Ndipo Farao anauka. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Ndipo ng'ombe zazikazi za maonekedwe oipa ndi zoonda zinadya ng'ombe zazikazi zisanu ndi ziwiri za maonekedwe abwino ndi zonenepazo. Ndipo Farao anauka. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Tsono ng'ombe zoondazo zidadya zinzake zonenepa zija. Pamenepo Farao adadzuka. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Ndipo ngʼombe zosaoneka bwino ndi zowonda zija zinadya ngʼombe zonenepa zija. Kenaka Farao anadzidzimuka. |
Ndipo, taonani, zinatuluka m'mtsinjemo ng'ombe zazikazi zisanu ndi ziwiri za maonekedwe okoma ndi zonenepa; ndipo zinadya mabango.
Ndipo, taonani ng'ombe zazikazi zisanu ndi ziwiri zinatuluka m'mtsinjemo pambuyo pao, za maonekedwe oipa ndi zoonda; ndipo zinaima pa ng'ombe zinazo m'mphepete mwa mtsinje.
Ndipo anagona nalotanso kachiwiri; ndipo taonani, ngala zisanu ndi ziwiri za tirigu zinamera pa mbuwa imodzi, zonenepa ndi zabwino.
Ndipo Solomoni anauka, ndipo taona, ndilo loto; nabwera ku Yerusalemu, naima ku likasa la chipangano cha Yehova, napereka nsembe zopsereza ndi nsembe zamtendere, nakonzera anyamata ake onse madyerero.