ndipo ng'ombe zazikazi zoonda ndi za maonekedwe oipa zinadya ng'ombe zazikazi zisanu ndi ziwiri zonenepa.
Genesis 41:21 - Buku Lopatulika Ndipo pamene zinadya sizinadziwike kuti zinadya; koma zinaipabe m'maonekedwe ao monga poyamba. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Ndipo pamene zinadya sizinadziwika kuti zinadya; koma zinaipabe m'maonekedwe ao monga poyamba. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Koma zitadya zinzakezo, palibe ndi mmodzi yemwe akadazindikira, popeza kuti ng'ombe zoondazo sizidasinthike konse kaonekedwe kake, koma zidangokhala zoonda ndithu monga kale. Tsono ndidadzuka. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Koma ngakhale ngʼombezi zinadya zinazo, palibe amene akanatha kuzindikira kuti zinatero popeza zinali zosaonekabe bwino monga poyamba. Ndipo ndinadzidzimuka. |
ndipo ng'ombe zazikazi zoonda ndi za maonekedwe oipa zinadya ng'ombe zazikazi zisanu ndi ziwiri zonenepa.
Pamenepo ndinauka. Ndipo ndinaona m'kulota kwanga, taona, ngala zisanu ndi ziwiri zinamera pa mbuwa imodzi zodzala ndi zabwino;
Ndipo, taonani ng'ombe zazikazi zisanu ndi ziwiri zinatuluka m'mtsinjemo pambuyo pao, za maonekedwe oipa ndi zoonda; ndipo zinaima pa ng'ombe zinazo m'mphepete mwa mtsinje.
Ndipo wina adzakwatula ndi dzanja lamanja, nakhala ndi njala; ndipo adzadya ndi dzanja lamanzere, osakhutai; iwo adzadya munthu yense nyama ya mkono wake wa iye mwini.
Nati kwa ine, Wobadwa ndi munthu iwe, dyetsa m'mimba mwako, nudzaze matumbo ako ndi mpukutu uwu ndakupatsawu. M'mwemo ndinaudya, ndi m'kamwa mwanga munazuna ngati uchi.