Ndipo panali zitapita zaka ziwiri zamphumphu, Farao analota; ndipo, taonani, anaima pamtsinje.
Genesis 41:2 - Buku Lopatulika Ndipo, taonani, zinatuluka m'mtsinjemo ng'ombe zazikazi zisanu ndi ziwiri za maonekedwe okoma ndi zonenepa; ndipo zinadya mabango. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Ndipo, taonani, zinatuluka m'nyanja ng'ombe zazikazi zisanu ndi ziwiri za maonekedwe okoma ndi zonenepa; ndipo zinadya mabango. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Nthaŵi yomweyo adangoona ng'ombe zisanu ndi ziŵiri zonenepa bwino zikutuluka mumtsinjemo, nkuyamba kudya msipu wam'mabango. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero ndipo anangoona ngʼombe zazikazi zisanu ndi ziwiri zooneka bwino ndi zonenepa zikutuluka mu mtsinje muja ndi kuyamba kudya msipu wa mu mawango. |
Ndipo panali zitapita zaka ziwiri zamphumphu, Farao analota; ndipo, taonani, anaima pamtsinje.
ndipo taona, zinatuluka m'mtsinjemo ng'ombe zazikazi zisanu ndi ziwiri, zonenepa ndi za maonekedwe abwino; ndipo zinadya m'mabango;
Ndipo, taonani ng'ombe zazikazi zisanu ndi ziwiri zinatuluka m'mtsinjemo pambuyo pao, za maonekedwe oipa ndi zoonda; ndipo zinaima pa ng'ombe zinazo m'mphepete mwa mtsinje.
Ndipo timitsinje tidzanunkha; mitsinje ya Ejipito idzachepa, nuima; bango ndi mlulu zidzafota.
Madambo oyandikana ndi mtsinje, pafupi ndi gombe la mtsinje, ndi zonse zobzala pamtsinje zidzauma, ndipo zidzachotsedwa, osakhalamo konse.