Baibulo la pa intaneti

Zotsatsa


Baibulo lonse Chipangano Chakale Chipangano Chatsopano




Genesis 39:8 - Buku Lopatulika

Koma iye anakana, nati kwa mkazi wa mbuyake, Taonani, mbuyanga sadziwa chimene chili ndi ine m'nyumbamu, ndipo anaika zake zonse m'manja anga;

Onani mutuwo

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

Koma iye anakana, nati kwa mkazi wa mbuyake, Taonani, mbuyanga sadziwa chimene chili ndi ine m'nyumbamu, ndipo anaika zake zonse m'manja anga;

Onani mutuwo

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

Yosefe adakana, adati, “Chifukwa choti ine ndikugwira ntchito muno, bwana wanga salabadiranso kanthu kalikonse ka m'nyumba muno. Adandipatsa ukapitao woyang'anira zake zonse,

Onani mutuwo

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

Koma iye anakana namuwuza kuti, “Inu mukuona kuti mbuye wanga sadandaula ndi kena kalikonse mʼnyumba muno, ndipo chawo chilichonse anachiyika mʼmanja mwanga.

Onani mutuwo



Genesis 39:8
15 Mawu Ofanana  

Woyang'anira m'kaidi sanayang'anire kanthu kalikonse kamene kanali m'manja a Yosefe, chifukwa Yehova anali ndi iye; ndipo zimene anazichita, Yehova anazipindulitsa.


Ndipo Yosefe anapeza ufulu pamaso pake, ndipo anamtumikira iye; ndipo anamuyesa iye woyang'anira pa nyumba yake, naika m'manja mwake zonse anali nazo.


Mwananga, akakukopa ochimwa usalole.


Woyanjana ndi ambiri angodziononga; koma lilipo bwenzi lipambana ndi mbale kuumirira.


Pakuti nzeru idzalowa m'mtima mwako, moyo wako udzakondwera ndi kudziwa,


M'kamwa mwa mkazi wachiwerewere muli dzenje lakuya; yemwe Yehova amkwiyira adzagwamo.


Chomwecho wolowa kwa mkazi wa mnzake; womkhudzayo sadzapulumuka chilango.


Kuti zikutchinjirizire kwa mkazi wachiwerewere, kwa mlendo wamkazi wosyasyalika ndi mau ake.