Ndipo anati, Ndinamva mau anu m'mundamu, ndipo ndinaopa chifukwa ndinali wamaliseche ine; ndipo ndinabisala.
Genesis 3:11 - Buku Lopatulika Ndipo anati, Ndani anakuuza iwe kuti uli wamaliseche? Kodi wadya za mtengo uja, umene ndinakuuza iwe kuti usadye? Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Ndipo anati, Ndani anakuuza iwe kuti uli wamaliseche? Kodi wadya za mtengo uja, umene ndinakuuza iwe kuti usadye? Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Mulungu adamufunsa kuti, “Kodi adakuuza ndani kuti uli maliseche? Kapena wadyatu zipatso za mtengo uja ndidakuuza kuti usadyewu eti?” Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Ndipo anamufunsa, “Ndani anakuwuza kuti uli maliseche? Kodi wadya zipatso za mtengo umene ndinakulamulira kuti usadye?” |
Ndipo anati, Ndinamva mau anu m'mundamu, ndipo ndinaopa chifukwa ndinali wamaliseche ine; ndipo ndinabisala.
Ndipo anati mwamunayo, Mkazi amene munandipatsa ine kuti akhale ndi ine, ameneyo anandipatsa ine za mtengo, ndipo ndinadya.
Izi unazichita iwe, ndipo ndinakhala chete Ine; unayesa kuti ndifanana nawe, ndidzakudzudzula, ndi kuchilongosola pamaso pako.
chifukwa kuti pamaso pake palibe munthu adzayesedwa wolungama ndi ntchito za lamulo; pakuti uchimo udziwika ndi lamulo.