Ndipo anamanga kumeneko guwa la nsembe, naitana dzina la Yehova, namanga hema wake kumeneko: ndi pamenepo anyamata a Isaki anakumba chitsime.
Genesis 26:32 - Buku Lopatulika Ndipo panali tsiku lomwelo anyamata ake a Isaki anadza namuuza iye za chitsime chimene anakumba, nati kwa iye, Tapeza madzi. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Ndipo panali tsiku lomwelo anyamata ake a Isaki anadza namuuza iye za chitsime chimene anakumba, nati kwa iye, Tapeza madzi. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Tsiku limenelo antchito ake a Isaki adabwera kudzamuuza za chitsime chimene iwowo adaakumba. Adati, “Tapeza madzi.” Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Tsiku limenelo, antchito a Isake anabwera namuwuza za chitsime chimene anakumba. Iwo anati, “Tawapeza madzi!” |
Ndipo anamanga kumeneko guwa la nsembe, naitana dzina la Yehova, namanga hema wake kumeneko: ndi pamenepo anyamata a Isaki anakumba chitsime.
Ndipo analawira m'mamawa nalumbirirana wina ndi mnzake; ndipo Isaki anawalola amuke, ndipo anauka kuchokera kwa iye m'mtendere.
Ndipo anatcha dzina lake Siba, chifukwa chake dzina la mzindawo ndi Beereseba kufikira lero lino.
Pemphani, ndipo chidzapatsidwa kwa inu; funani, ndipo mudzapeza; gogodani, ndipo chidzatsegulidwa kwa inu;