ukatero udzakhala wosachimwa pa malumbiro ako, pofika iwe kwa abale anga; ndipo ngati sadzakupatsa iwe, udzakhala wosachimwa pa malumbiro ako.
Genesis 24:8 - Buku Lopatulika Ndipo ngati sadzafuna mkaziyo kukutsata iwe, udzakhala wosachimwa pa chilumbiro changachi: koma mwana wanga usambwezerenso kumeneko. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Ndipo ngati sadzafuna mkaziyo kukutsata iwe, udzakhala wosachimwa pa chilumbiro changachi: koma mwana wanga usambwezerenso kumeneko. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Koma ngati mkaziyo adzakana kubwera nawe kuno, udzamasuka ku lumbiro limeneli. Komabe mwa njira iliyonse, mwana wanga usadzapite naye kuti akakhale kumeneko.” Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Ngati mkaziyo adzakana kubwerera nawe ndiye kuti udzakhala womasuka ku lumbiro langa. Koma usadzamutenge mwana wanga ndi kubwerera naye kumeneko.” |
ukatero udzakhala wosachimwa pa malumbiro ako, pofika iwe kwa abale anga; ndipo ngati sadzakupatsa iwe, udzakhala wosachimwa pa malumbiro ako.
Koma atate wake akamletsa tsiku lakumva iye; zowinda zake zonse, ndi zodziletsa zake zonse anamanga nazo moyo wake, sizidzakhazikika; ndipo Yehova adzamkhululukira, popeza atate wake anamletsa.
Koma mwamuna wake akamletsa tsiku lakumva iye; pamenepo adzafafaniza chowinda chake anali nacho, ndi zonena zopanda pake za milomo yake, zimene anamanga nazo moyo wake; ndipo Yehova adzamkhululukira.
Ndipo Stefano anati, Amuna inu, abale, ndi atate, tamverani. Mulungu wa ulemerero anaonekera kwa kholo lathu Abrahamu, pokhala iye mu Mesopotamiya, asanayambe kukhala mu Harani;
Tidzawachitira ichi, ndi kuwasunga amoyo; ungatigwere mkwiyo chifukwa cha lumbirolo tidawalumbirira.