Ndipo anati kwa iye mnyamatayo, Kapena sadzafuna mkaziyo kunditsata ine ku dziko lino: kodi ndikambwezerenso mwana wanu ku dziko komwe mwachokera inu?
Genesis 24:6 - Buku Lopatulika Ndipo Abrahamu anati kwa iye, Chenjera iwe, usambwezerenso mwana wanga kumeneko. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Ndipo Abrahamu anati kwa iye, Chenjera iwe, usambwezerenso mwana wanga kumeneko. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Abrahamu adayankha kuti, “Usadzamperekeze kumeneko mwana wangayo. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Abrahamu anati, “Uwonetsetse kuti usadzabwerere naye mwana wanga kumeneko. |
Ndipo anati kwa iye mnyamatayo, Kapena sadzafuna mkaziyo kunditsata ine ku dziko lino: kodi ndikambwezerenso mwana wanu ku dziko komwe mwachokera inu?
Ndipo ngati sadzafuna mkaziyo kukutsata iwe, udzakhala wosachimwa pa chilumbiro changachi: koma mwana wanga usambwezerenso kumeneko.
Khristu anatisandutsa mfulu, kuti tikhale mfulu; chifukwa chake chilimikani, musakodwenso ndi goli la ukapolo.
Koma ife si ndife a iwo akubwerera kulowa chitayiko; koma a iwo a chikhulupiriro cha ku chipulumutso cha moyo.
Ndi chikhulupiriro anakhala mlendo kudziko la lonjezano, losati lake, nakhalira m'mahema pamodzi ndi Isaki ndi Yakobo, olowa nyumba pamodzi ndi iye a lonjezano lomwelo;