Ndipo Abimeleki anati, Taona dziko langa lili pamaso pako; kumene kuli kwabwino pamaso pako takhala kumeneko.
Genesis 24:51 - Buku Lopatulika Taonani, Rebeka ali pamaso pako, mtenge ndi kumuka, akhale mkazi wa mwana wa mbuyako, monga wanena Yehova. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Taonani, Rebeka ali pamaso pako, mtenge ndi kumuka, akhale mkazi wa mwana wa mbuyako, monga wanena Yehova. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Nayu, Rebeka ndi ameneyu, mtengeni muzipita naye. Mukampereke kwa mwana wa mbuyanuyo kuti akakhale mkazi wake, monga momwe Chauta adanenera.” Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Nayu Rebeka, mutengeni muzipita naye kuti akakhale mkazi wa mwana wa mbuye wanu, monga Yehova wanenera.” |
Ndipo Abimeleki anati, Taona dziko langa lili pamaso pako; kumene kuli kwabwino pamaso pako takhala kumeneko.
Ndipo panali, asanathe kunena, taonani, anatuluka Rebeka, amene anambala Betuele, mwana wamwamuna wa Milika, mkazi wa Nahori mphwake wa Abrahamu, ndi mtsuko wake paphewa pake.
Ndipo anayankha Labani ndi Betuele, nati, Chatuluka kwa Yehova chinthu ichi; sitingathe kunena ndi iwe choipa kapena chabwino.
Mfumu niti, Ndili ndi chiyani ndi inu, ana a Zeruya? Pakuti atukwana, ndi pakuti Yehova ananena naye, Utukwane Davide; ndani tsono adzanena, Watero chifukwa ninji?
tengani akazi, balani ana aamuna ndi aakazi; kwatitsani ana anu aamuna, patsani ananu aakazi kwa amuna, kuti abale ana aamuna ndi aakazi; kuti mubalane pamenepo musachepe.