Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Genesis 24:50 - Buku Lopatulika

50 Ndipo anayankha Labani ndi Betuele, nati, Chatuluka kwa Yehova chinthu ichi; sitingathe kunena ndi iwe choipa kapena chabwino.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

50 Ndipo anayankha Labani ndi Betuele, nati, Chatuluka kwa Yehova chinthu ichi; sitingathe kunena ndi iwe choipa kapena chabwino.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

50 Pamenepo Labani ndi Betuele adauza munthuyo kuti, “Popeza kuti zimenezi nzochokera kwa Chauta, ife sitingachitepo kanthu.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

50 Labani ndi Betueli anayankha nati, “Izi ndi zochokera kwa Yehova, ndipo ife sitinganenepo kanthu.

Onani mutuwo Koperani




Genesis 24:50
15 Mawu Ofanana  

Ndipo panali, asanathe kunena, taonani, anatuluka Rebeka, amene anambala Betuele, mwana wamwamuna wa Milika, mkazi wa Nahori mphwake wa Abrahamu, ndi mtsuko wake paphewa pake.


Namwaliyo ndipo anathamanga nawauza zimenezo kunyumba ya amake.


Taonani, Rebeka ali pamaso pako, mtenge ndi kumuka, akhale mkazi wa mwana wa mbuyako, monga wanena Yehova.


Ndipo mnyamatayo anatulutsa zokometsera zasiliva ndi zagolide, ndi zovala, nampatsa Rebeka: ndipo anapatsa za mtengo wapatali kwa mlongo wake ndi amake.


Ndipo mlongo wake ndi amake anati, Namwali akhale ndi ife masiku akuwerengeka, afikire khumi; patsogolo pake iye adzamuka.


Ndipo anamdalitsa Rebeka, nati kwa iye, Mlongo wathu ndiwe, iwe ukhale amai wa anthu zikwizikwi, mbeu zako zigonjetse chipata cha iwo akudana nao.


Ndipo Mulungu anadza kwa Labani Mwaramu usiku, nati kwa iye, Tadziyang'anira wekha, usanene kwa Yakobo kapena zabwino kapena zoipa.


M'dzanja langa muli mphamvu yakuchitira iwe zoipa koma Mulungu wa atate wako anati kwa ine usiku walero, kuti, Tadziyang'anira wekha, usanene kwa Yakobo kapena zabwino kapena zoipa.


Ndipo Abisalomu sanalankhule ndi Aminoni chabwino kapena choipa, pakuti Abisalomu anamuda Aminoni popeza adachepetsa mlongo wake Tamara.


Potero mfumu siinamvere anthuwo, pakuti kusintha uku kunachokera kwa Yehova, kuti akhazikitse mau ake amene Yehova ananenetsa Ahiya wa ku Silo kwa Yerobowamu mwana wa Nebati.


Yehova atero, Musamuka, ndipo musakayambana ndi abale anu ana a Israele, bwererani yense kunyumba kwake; popeza chinthuchi chachokera kwa Ine. Ndipo iwo anamvera mau a Yehova, natembenuka, nabwerera monga mwa mau a Yehova.


Ichi chidzera kwa Yehova; nchodabwitsa ichi pamaso pathu.


Yesu ananena kwa iwo, Kodi simunawerenge konse m'malembo, Mwala umene anaukana omanga nyumba womwewu unakhala mutu wa pangodya: Ichi chinachokera kwa Ambuye, ndipo chili chozizwitsa m'maso mwathu?


Ichi chinachokera kwa Ambuye, ndipo chili chozizwitsa m'maso mwathu?


Ngati tsono Mulungu anawapatsa iwo mphatso yomweyi yonga ya kwa ife, pamene tinakhulupirira Ambuye Yesu Khristu, ndine yani kuti ndingathe kuletsa Mulungu?


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa