Ndipo Loti anatukula maso ake nayang'ana chigwa chonse cha Yordani kuti chonsecho chinali ndi madzi ambiri, asanaononge Yehova Sodomu ndi Gomora, monga munda wa Yehova, monga dziko la Ejipito pakunka ku Zowari.
Genesis 2:8 - Buku Lopatulika Ndipo Yehova Mulungu anabzala m'munda ku Edeni chakum'mawa; momwemo ndipo adaika munthu adamuumbayo. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Ndipo Yehova Mulungu anabzala m'munda ku Edeni chakum'mawa; momwemo ndipo adaika munthu adamuumbayo. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Kenaka Chauta adatsekula munda mu Edeni chakuvuma, ndipo munthu adamuumbayo adamkhazika m'menemo. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Kenaka Yehova Mulungu anatsekula munda wa Edeni chakummawa; kumeneko anayikako munthu amene anamupanga uja. |
Ndipo Loti anatukula maso ake nayang'ana chigwa chonse cha Yordani kuti chonsecho chinali ndi madzi ambiri, asanaononge Yehova Sodomu ndi Gomora, monga munda wa Yehova, monga dziko la Ejipito pakunka ku Zowari.
Yehova Mulungu anamtulutsa iye m'munda wa Edeni, kuti alime nthaka m'mene anamtenga iye.
Ndipo anamuingitsa munthuyo; nakhazika akerubi cha kum'mawa kwake kwa munda wa Edeni, ndi lupanga lamoto lakuzungulira ponsepo, lakusunga njira ya ku mtengo wa moyo.
Ndipo Kaini anatuluka pamaso pa Yehova, ndipo anakhala m'dziko la Nodi, kum'mawa kwake kwa Edeni.
Kodi milungu ya amitundu inawalanditsa amene makolo anga anawaononga, ndiwo Gozani, ndi Harani Rezefe, ndi ana a Edeni okhala mu Telasara?
Pakuti Yehova watonthoza mtima wa Ziyoni, watonthoza mtima wa malo ake onse abwinja; ndipo wasandutsa chipululu chake ngati Edeni, ndi malo ake ouma ngati munda wa Yehova; kukondwa ndi kusangalala kudzapezedwa m'menemo, mayamikiro, ndi mau a nyimbo yokoma.
Harani ndi Kane ndi Edeni, amalonda a ku Sheba Asiriya ndi Kilimadi, anagulana nawe malonda.
Unali mu Edeni, munda wa Mulungu, mwala uliwonse wa mtengo wake unali chofunda chako, sardiyo, topazi, diamondi, berulo, sohamu, ndi yaspi, safiro, nofeki, bareketi, ndi golide; malingaka ako ndi akazi ako anakutumikira tsiku lolengedwa iwe zinakonzekeratu.
Ndinagwedeza amitundu ndi phokoso la kugwa kwake, muja ndinagwetsera kumanda, pamodzi ndi iwo otsikira kumanda; ndi mitengo yonse ya ku Edeni yosankhika, ndi yokometsetsa ya ku Lebanoni, yonse yakumwa madzi, inasangalala munsi mwake mwa dziko lapansi.
Momwemo ufanana ndi yani mu ulemerero ndi ukulu pakati pa mitengo ya Edeni? Koma udzatsitsidwa pamodzi ndi mitengo ya Edeni m'munsi mwake mwa dziko lapansi, udzagona pakati pa osadulidwa, pamodzi ndi iwo ophedwa ndi lupanga. Uwu ndi Farao ndi aunyinji ake onse, ati Ambuye Yehova.
Moto unyambita pamaso pao, ndi m'mbuyo mwao litentha lawi la moto; kumaso kwao dziko likunga munda wa Edeni, koma m'mbuyo mwao likunga chipululu chopanda kanthu; palibenso wakuwapulumuka.