Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Genesis 3:23 - Buku Lopatulika

23 Yehova Mulungu anamtulutsa iye m'munda wa Edeni, kuti alime nthaka m'mene anamtenga iye.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

23 Yehova Mulungu anamtulutsa iye m'munda wa Edeni, kuti alime nthaka m'mene anamtenga iye.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

23 Motero Chauta adamtulutsamo m'munda mwa Edeni muja, kuti azilima m'nthaka momwe adachokera.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

23 Kotero Yehova Mulungu anatulutsa Adamu Mʼmunda wa Edeni kuti azilima mʼnthaka imene anachokera.

Onani mutuwo Koperani




Genesis 3:23
10 Mawu Ofanana  

Ndi zomera zonse za m'munda zisanakhale m'dziko lapansi, ndiponso matherere onse a m'munda asanamere; chifukwa Yehova Mulungu sanavumbitsire mvula padziko lapansi, ndipo panalibe munthu wakulima nthaka;


Ndipo Yehova Mulungu anaumba munthu ndi dothi lapansi, nauzira mpweya wa moyo m'mphuno mwake; munthuyo nakhala wamoyo.


Ndipo Yehova Mulungu anabzala m'munda ku Edeni chakum'mawa; momwemo ndipo adaika munthu adamuumbayo.


m'thukuta la nkhope yako udzadya chakudya, kufikira kuti udzabwerera kunthaka: chifukwa kuti m'menemo unatengedwa: chifukwa kuti ndiwe fumbi, ndi kufumbiko udzabwerera.


Ndipo anati Yehova Mulungu, Taonani, munthuyo akhala ngati mmodzi wa ife, wakudziwa zabwino ndi zoipa: ndipo tsopano kuti asatambasule dzanja lake ndi kutenga za mtengo wa moyo, ndi kudya, ndi kukhala ndi moyo nthawi zonse,


Ndipo anamuingitsa munthuyo; nakhazika akerubi cha kum'mawa kwake kwa munda wa Edeni, ndi lupanga lamoto lakuzungulira ponsepo, lakusunga njira ya ku mtengo wa moyo.


pamene udzalima panthaka siidzaperekanso kwa iwe mphamvu yake: udzakhala wothawathawa ndi woyendayenda padziko lapansi.


Ndipo anabalanso mphwake Abele. Abele anakhala mbusa wa nkhosa, koma Kaini anali wakulima nthaka.


Ndipo anayamba Nowa kukhala munthu wakulima nthaka, ndipo analima munda wampesa:


Phindutu la dziko lipindulira onse; ngakhale mfumu munda umthandiza;


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa