Yehova Mulungu ndipo anati, Si kwabwino kuti munthu akhale yekha; ndidzampangira womthangatira iye.
Genesis 2:20 - Buku Lopatulika Adamu ndipo anazitcha maina zinyama zonse, ndi mbalame za m'mlengalenga ndi zamoyo zonse za m'thengo: koma kwa Adamu sanapezeke womthangatira iye. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Adamu ndipo anazitcha maina zinyama zonse, ndi mbalame za m'mlengalenga ndi zamoyo zonse za m'thengo: koma kwa Adamu sanapezedwa womthangatira iye. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Adamu adazitcha maina nyama zonse, mbalame ndi zamoyo zonse zakuthengo. Komabe panalibe mnzake woti azimthandiza. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Choncho Adamu anazitcha mayina ziweto zonse, mbalame zamlengalenga ndi nyama zakuthengo zonse. Komabe munthu uja analibe mnzake womuthandiza. |
Yehova Mulungu ndipo anati, Si kwabwino kuti munthu akhale yekha; ndidzampangira womthangatira iye.
Koma Yehova Mulungu anamgonetsa Adamu tulo tatikulu, ndipo anagona; ndipo anatengako nthiti yake imodzi, natsekapo ndi mnofu pamalo pake.