Genesis 15:12 - Buku Lopatulika Ndipo linalinkulowa dzuwa, ndi tulo tatikulu tinamgwera Abramu: ndipo taonani, kuopsa kwa mdima waukulu kunamgwera iye. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Ndipo linalinkulowa dzuwa, ndi tulo tatikulu tinamgwera Abramu: ndipo taonani, kuopsa kwa mdima waukulu kunamgwera iye. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Pamene dzuŵa linkaloŵa, Abramu adagwidwa ndi tulo tofanato, ndiponso adachita mantha kwambiri. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Pamene dzuwa limalowa Abramu anagona tulo tofa nato ndipo mdima wandiweyani ndi wochititsa mantha unamuphimba. |
Koma Yehova Mulungu anamgonetsa Adamu tulo tatikulu, ndipo anagona; ndipo anatengako nthiti yake imodzi, natsekapo ndi mnofu pamalo pake.
Ndipo anafika kumalo, nagona kumeneko usiku, chifukwa lidalowa dzuwa: ndipo anatenga mwala wa kumeneko, nauika pansi pamutu wake, nagona tulo kumeneko.
M'kulota, m'masomphenya a usiku, pakuwagwera anthu tulo tatikulu, pogona mwatcheru pakama,
Ndipo mnyamata dzina lake Yutiko anakhala pazenera, wogwidwa nato tulo tatikulu; ndipo pakukhala chifotokozere Paulo, ndipo pogwidwa nato tulo, anagwa posanja pachiwiri, ndipo anamtola wakufa.
Chomwecho Davide anatenga mkondowo, ndi chikho cha madzi ku mutu wa Saulo nachoka iwowa, osawaona munthu, kapena kuzidziwa, kapena kugalamuka; pakuti onse anali m'tulo; popeza tulo tatikulu tochokera kwa Yehova tinawagwira onse.