Baibulo la pa intaneti

Zotsatsa


Baibulo lonse Chipangano Chakale Chipangano Chatsopano




Genesis 14:4 - Buku Lopatulika

Zaka khumi ndi ziwiri iwo anamtumikira Kedorilaomere, chaka chakhumi ndi chitatu anapanduka.

Onani mutuwo

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

Zaka khumi ndi ziwiri iwo anamtumikira Kedorilaomere, chaka chakhumi ndi chitatu anapanduka.

Onani mutuwo

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

Kedorilaomere ndiye ankalamulira onseŵa pa zaka khumi ndi ziŵiri, koma chaka chakhumi ndi chitatu onseŵa adamuukira.

Onani mutuwo

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

Kwa zaka khumi ndi ziwiri anali pansi pa ulamuliro wa Kedorilaomere, koma mʼchaka cha khumi ndi chitatu anamuwukira.

Onani mutuwo



Genesis 14:4
5 Mawu Ofanana  

Ndipo panali masiku a Amurafere mfumu ya Sinara, ndi Ariyoki mfumu ya Elasara, ndi Kedorilaomere mfumu ya Elamu, ndi Tidala mfumu ya Goimu,


Onse amenewo anadziphatikana pa chigwa cha Sidimu (pamenepo ndi pa Nyanja ya Mchere).


Chaka chakhumi ndi chinai ndipo anadza Kedorilaomere ndi mafumu amene anali naye, nawakantha Arefaimu mu Asiteroti-Karanaimu, ndi Azuzimu mu Hamu, ndi Aemimu mu Savekiriyataimu,


Koma anapandukira ndi kutuma mithenga yake ku Ejipito, kuti ampatse akavalo ndi anthu ambiri. Adzapindula kodi? Adzapulumuka wakuchita izi? Athyole pangano ndi kupulumuka kodi?