Genesis 1:18 - Buku Lopatulika zilamulire usana ndi usiku, zilekanitse kuyera ndi mdima: ndipo anaona Mulungu kuti kunali kwabwino. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Nizilamulire usana ndi usiku, nizilekanitse kuyera ndi mdima: ndipo anaona Mulungu kuti kunali kwabwino. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa kuti iziŵala usana ndi usiku, kulekanitsa kuyera ndi mdima. Mulungu adaona kuti zinali zabwino. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero kuti zilamulire usana ndi usiku, ndi kuti zilekanitse kuwala ndi mdima. Mulungu anaona kuti zinali bwino. |
Kutuluka kwake lituluka kolekezera thambo, ndipo kuzungulira kwake lifikira ku malekezero ake; ndipo kulibe kanthu kobisalira kutentha kwake.
Yehova atero, amene apatsa dzuwa kuti liunikire usana, ndi malemba a mwezi ndi a nyenyezi kuti aunikire usiku, amene atonthoza nyanja, pamene mafunde ake agavira; Yehova wa makamu ndi dzina lake: