Ndipo dziko lapansi linamera udzu, therere lobala mbeu monga mwa mtundu wake, ndi mtengo wakubala zipatso, momwemo muli mbeu yake, monga mwa mtundu wake; ndipo anaona Mulungu kuti kunali kwabwino.
Genesis 1:13 - Buku Lopatulika Ndipo panali madzulo ndipo panali m'mawa, tsiku lachitatu. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Ndipo panali madzulo ndipo panali m'mawa, tsiku lachitatu. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Ndipo kudali madzulo ndiponso m'maŵa, tsiku lachitatu. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Ndipo panali madzulo ndiponso mmawa pa tsiku lachitatu. |
Ndipo dziko lapansi linamera udzu, therere lobala mbeu monga mwa mtundu wake, ndi mtengo wakubala zipatso, momwemo muli mbeu yake, monga mwa mtundu wake; ndipo anaona Mulungu kuti kunali kwabwino.
Ndipo Mulungu anati, Pakhale zounikira pathambo la kumwamba, zakulekanitsa usana ndi usiku; zikhale zizindikiro ndi nyengo, ndi masiku, ndi zaka;
Ndipo anaziona Mulungu zonse zimene adazipanga, ndipo, taonani, zinali zabwino ndithu. Ndipo panali madzulo ndipo panali m'mawa, tsiku lachisanu ndi chimodzi.
Ndipo Mulungu anatcha kuyerako Usana, ndi mdimawo anautcha Usiku. Ndipo panali madzulo ndipo panali m'mawa, tsiku loyamba.
Ndipo Mulungu analitcha thambolo Kumwamba. Ndipo panali madzulo ndipo panali m'mawa, tsiku lachiwiri.
Ndipo Yesu ananena naye, Ndithu ndinena ndi iwe, kuti lero, usiku uno, tambala asanalire kawiri, udzandikana Ine katatu.