Baibulo la pa intaneti

Zotsatsa


Baibulo lonse Chipangano Chakale Chipangano Chatsopano




Eksodo 9:9 - Buku Lopatulika

Ndipo lidzakhala fumbi losalala padziko lonse la Ejipito, ndipo lidzakhala pa anthu ndi pa zoweta ngati zilonda zobuka ndi matuza, m'dziko lonse la Ejipito.

Onani mutuwo

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

Ndipo lidzakhala fumbi losalala pa dziko lonse la Ejipito, ndipo lidzakhala pa anthu ndi pa zoweta ngati zilonda zobuka ndi matuza, m'dziko lonse la Ejipito.

Onani mutuwo

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

Phulusalo lidzaulukira m'dziko lonse la Ejipito ngati fumbi. Ndipo konse kumene lidzaulukireko, kudzabuka zithupsa zomaphulika ndi kusanduka zilonda pa anthu ndi pa nyama zomwe.”

Onani mutuwo

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

Phulusalo lidzasanduka fumbi pa dziko lonse la Igupto. Tsono fumbilo lidzasanduka zithupsa zomaphulika nʼkukhala zilonda pa munthu aliyense ndi pa nyama zomwe mʼdziko lonse la Igupto.”

Onani mutuwo



Eksodo 9:9
7 Mawu Ofanana  

Natuluka Satana pamaso pa Yehova, nazunza Yobu ndi zilonda zowawa, kuyambira kuphazi lake kufikira pakati pamutu pake.


Ndipo anatenga phulusa la m'ng'anjo, naima pamaso pa Farao; ndi Mose analiwaza kuthambo; ndipo linakhala zilonda zobuka ndi matuza pa anthu ndi pa zoweta.


Ndipo Yehova ananena ndi Mose ndi Aroni, Tengani phulusa la ng'anjo lodzala manja; ndi Mose aliwaze kuthambo pamaso pa Farao.


Yehova adzakukanthani ndi zilombo za ku Ejipito, ndi nthenda yotuluka mudzi, ndi chipere, ndi mphere, osachira nazo.


Yehova adzakukanthani ndi chilonda choipa chosachira nacho kumaondo, ndi kumiyendo, kuyambira pansi pa phazi lanu kufikira pamwamba pamutu panu.


Ndipo anachoka woyamba, natsanulira mbale yake kudziko; ndipo kunakhala chilonda choipa ndi chosautsa pa anthu akukhala nalo lemba la chilombo nalambira fano lake.