Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -




Chivumbulutso 16:2 - Buku Lopatulika

2 Ndipo anachoka woyamba, natsanulira mbale yake kudziko; ndipo kunakhala chilonda choipa ndi chosautsa pa anthu akukhala nalo lemba la chilombo nalambira fano lake.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

2 Ndipo anachoka woyamba, natsanulira mbale yake kudziko; ndipo kunakhala chilonda choipa ndi chosautsa pa anthu akukhala nalo lemba la chilombo nalambira fano lake.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

2 Motero mngelo woyamba adakakhuthulira za mumkhate mwake pa dziko lapansi. Pamenepo zilonda zonyansa ndi zopweteka zidabuka pa anthu onse aja, amene adaalembedwa chizindikiro cha chilombo chija, napembedza fano lake.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

2 Mngelo woyamba anapita natsanula mbale yake pa dziko lapansi ndipo zilonda zoyipa ndi zowawa zinabuka pa anthu amene anali ndi chizindikiro cha chirombo chija, napembedza fano lake.

Onani mutuwo Koperani




Chivumbulutso 16:2
22 Mawu Ofanana  

ndipo mudzadwala kwakukulu nthenda yamatumbo, mpaka matumbo anu adzatuluka chifukwa cha nthendayi tsiku ndi tsiku.


Ndi pambuyo pake pa izi zonse Yehova anamdwalitsa m'matumbo ake ndi nthenda yosachira nayo.


Anaombetsa m'mwamba mphepo ya kum'mawa, natsogoza mwera ndi mphamvu yake.


chifukwa chake Ambuye adzachita nkanambo pa liwombo la ana aakazi a Ziyoni, ndipo Yehova adzavundukula m'chuuno mwao.


Ndipo padzakhala m'malo mwa zonunkhiritsa mudzakhala zovunda; ndi m'malo mwa lamba chingwe; ndipo m'malo mwa tsitsi labwino dazi; m'malo mwa chovala chapachifuwa mpango wachiguduli; zipsera m'malo mwa ukoma.


Ndipo pomwepo mngelo wa Ambuye anamkantha, chifukwa sanampatse Mulungu ulemerero; ndipo anadyedwa ndi mphutsi, natsirizika.


Yehova adzakukanthani ndi zilombo za ku Ejipito, ndi nthenda yotuluka mudzi, ndi chipere, ndi mphere, osachira nazo.


Yehova adzakukanthani ndi chilonda choipa chosachira nacho kumaondo, ndi kumiyendo, kuyambira pansi pa phazi lanu kufikira pamwamba pamutu panu.


Ndipo Yehova adzakuchotserani nthenda zonse; sadzakuikirani nthenda zoipa zilizonse za Aejipito muzidziwa zija; koma adzaziika pa onse akudana ndi inu.


Ndipo chichita ulamuliro wonse wa chilombo choyamba pamaso pake. Ndipo chilambiritsa dziko ndi iwo akukhala momwemo chilombo choyamba, chimene bala lake la kuimfa lidapola.


Ndipo Iye wokhala pamtambo anaponya chisenga chake padziko, ndipo dzinthu za dziko zinamwetedwa.


Ndipo anawatsata mngelo wina, wachitatu, nanena ndi mau aakulu, Ngati wina alambira chilombocho, ndi fano lake, nalandira lemba pamphumi pake, kapena padzanja lake


Ndipo ndinamva mau aakulu ochokera ku Kachisi, akunena kwa angelo asanu ndi awiri, Mukani, ndipo tsanulirani kudziko mbale zisanu ndi ziwiri za mkwiyo wa Mulungu.


nachitira mwano Mulungu wa mu Mwamba chifukwa cha zowawa zao ndi zilonda zao; ndipo sanalape ntchito zao.


Ndipo woyamba anaomba lipenga, ndipo panakhala matalala ndi moto, zosakaniza ndi mwazi, ndipo anazitaya padziko lapansi; ndipo limodzi la magawo atatu a dziko lidapserera, ndipo limodzi la magawo atatu a mitengo lidapserera, ndipo msipu wonse udapserera.


Koma Yehova anavuta iwo a ku Asidodi ndi dzanja lake, nawaononga, nawazunza ndi mafundo, mu Asidodi ndi m'midzi yake.


Ndipo kunali atafika nalo, dzanja la Yehova linatsutsa mzindawo ndi kusautsa kwakukulu; ndipo anazunza anthu a mzindawo, aakulu ndi aang'ono; ndi mafundo anawabuka.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa