Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -




Yobu 2:7 - Buku Lopatulika

7 Natuluka Satana pamaso pa Yehova, nazunza Yobu ndi zilonda zowawa, kuyambira kuphazi lake kufikira pakati pamutu pake.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

7 Natuluka Satana pamaso pa Yehova, nazunza Yobu ndi zilonda zowawa, kuyambira kuphazi lake kufikira pakati pamutu pake.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

7 Choncho Satana adachoka kumsiya Chauta napita kukazunza Yobe ndi zilonda zoopsa pa thupi lonse.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

7 Choncho Satana anachoka pamaso pa Yehova napita kukazunza Yobu ndi zilonda zaululu pa thupi lake lonse.

Onani mutuwo Koperani




Yobu 2:7
14 Mawu Ofanana  

Ndipo mu Israele monse munalibe wina anthu anamtama kwambiri chifukwa cha kukongola kwake monga Abisalomu; kuyambira ku mapazi kufikira pakati pamutu wake mwa iye munalibe chilema.


Nati, Ndidzatuluka, ndidzakhala mzimu wonama m'kamwa mwa aneneri ake onse. Nati, Udzamnyengadi, nudzakhozanso; tuluka, ukatero kumene.


Koma mutambasule dzanja lanu ndi kumkhudzira zake zonse, ndipo adzakuchitirani mwano pamaso panu.


Momwemo munthu akutha ngati chinthu choola, ngati chovala chodyedwa ndi njenjete.


Ndipo Yehova anati kwa Satana, Taona, akhale m'dzanja lako; moyo wake wokha uuleke.


Khungu langa lada, nilindifundukira; ndi mafupa anga awawa ndi kutentha kwao.


Mnofu wanga wavala mphutsi ndi nkanambo zadothi; khungu langa lang'ambika, nilinyansa.


Kuchokera pansi pa phazi kufikira kumutu m'menemo mulibe changwiro; koma mabala, ndi mikwingwirima, ndi zilonda; sizinapole, ngakhale kumangidwa, ngakhale kupakidwa mafuta.


chifukwa chake Ambuye adzachita nkanambo pa liwombo la ana aakazi a Ziyoni, ndipo Yehova adzavundukula m'chuuno mwao.


Yehova adzakukanthani ndi zilombo za ku Ejipito, ndi nthenda yotuluka mudzi, ndi chipere, ndi mphere, osachira nazo.


Yehova adzakukanthani ndi chilonda choipa chosachira nacho kumaondo, ndi kumiyendo, kuyambira pansi pa phazi lanu kufikira pamwamba pamutu panu.


nachitira mwano Mulungu wa mu Mwamba chifukwa cha zowawa zao ndi zilonda zao; ndipo sanalape ntchito zao.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa