Ndipo Solomoni anaimirira ku guwa la nsembe la Yehova pamaso pa msonkhano wonse wa Israele, natambasulira manja ake kumwamba, nati,
Eksodo 9:33 - Buku Lopatulika Ndipo Mose anatuluka kwa Farao m'mzinda nakweza manja ake kwa Yehova; ndipo mabingu ndi matalala analeka, ndi mvula siinavumbanso padziko. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Ndipo Mose anatuluka kwa Farao m'mudzi nasasatulira manja ake kwa Yehova; ndipo mabingu ndi matalala analeka, ndi mvula siinavumbanso padziko. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Mose adachoka kwa Farao kuja, natuluka mumzindamo. Ndipo adakweza manja ake kumwamba, napemphera kwa Chauta. Tsono mabingu aja ndi matalala adaleka, ndipo mvula idakata. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Mose anasiyana ndi Farao natuluka mu mzindawo. Iye anakweza manja ake kwa Yehova. Mabingu ndi matalala zinaleka, ndipo mvula inalekeratu kugwa mʼdzikolo. |
Ndipo Solomoni anaimirira ku guwa la nsembe la Yehova pamaso pa msonkhano wonse wa Israele, natambasulira manja ake kumwamba, nati,
Ndipo Mose ndi Aroni anatuluka kwa Farao; ndi Mose anafuulira kwa Yehova kunena za achule amene adawaika pa Farao.
Pamenepo Farao anaitana Mose ndi Aroni, nati, Mundipembere Yehova, kuti andichotsere ine ndi anthu anga achulewo; ndipo ndidzalola anthu amuke, kuti amphere Yehova nsembe.
Ndipo Mose ananena naye, Potuluka m'mzinda ine, ndidzakweza manja anga kwa Yehova; mabingu adzaleka, ndi matalala sadzakhalaponso; kuti mudziwe kuti dziko lapansi nla Yehova.
Pamene Farao anaona kuti mvula ndi matalala ndi mabingu zidaleka anaonjezanso kuchimwa, naumitsa mtima wake, iye ndi anyamata ake.