Perekani tsono mtima ndi moyo wanu kufunafuna Yehova Mulungu wanu; ndipo nyamukani ndi kumanga malo opatulika a Yehova Mulungu, kuti abwere nalo likasa la chipangano la Yehova, ndi zipangizo zopatulika za Mulungu, kunyumba imene idzamangidwira dzina la Yehova.
Ndipo Yehova anati kwa Mose, Tambasula dzanja lako kuthambo, kuti pakhale matalala padziko lonse la Ejipito, pa anthu ndi pa zoweta, ndi pa zitsamba zonse zakuthengo, m'dziko la Ejipito.
Ndipo munthuyu anati kwa ine, Wobadwa ndi munthu iwe, penya ndi maso ako, imva m'makutu mwako, nuike mtima wako pa zonse ndidzakuonetsa iwe; pakuti unatengedwa kudza kuno, kuti ndikuonetse izi; fotokozera nyumba ya Israele zonse uziona.
Pamenepo anati kwa ine, Usaope Daniele; pakuti kuyambira tsiku loyamba lija unaika mtima wako kuzindikira ndi kudzichepetsa pamaso pa Mulungu wako, mau ako anamveka; ndipo ndadzera mau ako.