Eksodo 8:31 - Buku Lopatulika Ndipo Yehova anachita monga mwa mau a Mose; nachotsera Farao ndi anyamata ake ndi anthu ake mizazayo, sunatsale ndi umodzi wonse. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Ndipo Yehova anachita monga mwa mau a Mose; nachotsera Farao ndi anyamata ake ndi anthu ake mizazayo, sunatsala ndi umodzi wonse. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Motero Chauta adachitadi monga momwe Mose adapemphera. Pomwepo mizaza idamchoka Farao ndi nduna zake ndi anthu ake omwe. Sudatsalepo ndi umodzi omwe. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Ndipo Yehova anachita zomwe Mose anapempha: Ntchentche zoluma zinachoka kwa Farao ndi nduna zake ndiponso kwa anthu ake. Palibe ngakhale imodzi yomwe inatsala. |
Pakuti ukapanda kulola anthu anga amuke, taona, ndidzatuma mizaza pa iwe, ndi pa anyamata ako, ndi pa anthu ako, ndi pa nyumba zako; ndipo nyumba za Aejipito zidzadzala nayo mizaza, ndi nthaka yomwe imene ikhalapo.
Ungayanje woipa, koma sadzaphunzira chilungamo; m'dziko la machitidwe oongoka, iye adzangochimwa, sadzaona chifumu cha Yehova.