Eksodo 8:30 - Buku Lopatulika Ndipo Mose anatuluka kwa Farao, napemba Yehova. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Ndipo Mose anatuluka kwa Farao, napemba Yehova. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Mose atachoka kwa Faraoko, adakapemphera kwa Chauta. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Choncho Mose anasiyana ndi Farao nakapemphera kwa Yehova. |
Ndipo Mose ndi Aroni anatuluka kwa Farao; ndi Mose anafuulira kwa Yehova kunena za achule amene adawaika pa Farao.
Ndipo Yehova anachita monga mwa mau a Mose; nachotsera Farao ndi anyamata ake ndi anthu ake mizazayo, sunatsale ndi umodzi wonse.
Ndipo Mose anatuluka kwa Farao m'mzinda nakweza manja ake kwa Yehova; ndipo mabingu ndi matalala analeka, ndi mvula siinavumbanso padziko.
Chifukwa chake muvomerezane wina ndi mnzake machimo anu, ndipo mupempherere wina kwa mnzake kuti muchiritsidwe. Pemphero la munthu wolungama likhoza kwakukulu m'machitidwe ake.