Baibulo la pa intaneti

Zotsatsa


Baibulo lonse Chipangano Chakale Chipangano Chatsopano




Eksodo 7:15 - Buku Lopatulika

Muka kwa Farao m'mawa; taona, atuluka kunka kumadzi; nuime kumlinda m'mbali mwa mtsinje; ndi ndodo idasanduka njokayo uigwire m'dzanja lako.

Onani mutuwo

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

Muka kwa Farao m'mawa; taona, atuluka kunka kumadzi; nuime kumlinda m'mbali mwa nyanja; ndi ndodo idasanduka njokayo uigwire m'dzanja lako.

Onani mutuwo

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

Upite m'maŵa ukakumane naye pamene akupita ku mtsinje wa Nailo. Ukamdikire pambali pa mtsinjewo. Tsono utenge ndodo ija idaasanduka njokayi.

Onani mutuwo

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

Upite kwa Farao mmawa pamene azidzapita ku madzi. Ukamudikire mʼmbali mwa Nailo kuti ukakumane naye ndipo unyamule ndodo imene inasanduka njoka ija mʼdzanja lako.

Onani mutuwo



Eksodo 7:15
7 Mawu Ofanana  

Sanalole munthu awasautse; ndipo anadzudzula mafumu chifukwa cha iwowa;


Ndipo mwana wamkazi wa Farao anatsikira kukasamba m'mtsinje; ndipo atsikana ake anayendayenda m'mbali mwa mtsinje; ndipo iye anaona kabokosi pakati pa mabango, natuma mdzakazi wake akatenge.


Ndipo Mose ndi Aroni analowa kwa Farao, nachita monga momwe Yehova adawalamulira; ndipo Aroni anaponya pansi ndodo yake pamaso pa Farao, ndi pamaso pa anyamata ake, ndipo inasanduka chinjoka.


Ndipo Yehova ananena ndi Mose, Walemera mtima wa Farao, akana kulola anthu apite.


Ndipo Yehova anati kwa Mose Uuke ulawire mamawa, nuime pamaso pa Farao; taona, atuluka kunka kumadzi; nunene naye, Atero Yehova, Lola anthu anga amuke, anditumikire.


nena, uziti, Atero Ambuye Yehova, Taona nditsutsana nawe, Farao mfumu ya Aejipito, ng'ona yaikulu yakugona m'kati mwa mitsinje yake, imene ikuti, Mtsinje wanga ndi wangatu, ndadzipangira ndekha uwu.