Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -




Eksodo 7:15 - Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

15 Upite kwa Farao mmawa pamene azidzapita ku madzi. Ukamudikire mʼmbali mwa Nailo kuti ukakumane naye ndipo unyamule ndodo imene inasanduka njoka ija mʼdzanja lako.

Onani mutuwo Koperani

Buku Lopatulika

15 Muka kwa Farao m'mawa; taona, atuluka kunka kumadzi; nuime kumlinda m'mbali mwa mtsinje; ndi ndodo idasanduka njokayo uigwire m'dzanja lako.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

15 Muka kwa Farao m'mawa; taona, atuluka kunka kumadzi; nuime kumlinda m'mbali mwa nyanja; ndi ndodo idasanduka njokayo uigwire m'dzanja lako.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

15 Upite m'maŵa ukakumane naye pamene akupita ku mtsinje wa Nailo. Ukamdikire pambali pa mtsinjewo. Tsono utenge ndodo ija idaasanduka njokayi.

Onani mutuwo Koperani




Eksodo 7:15
7 Mawu Ofanana  

Iye sanalole munthu aliyense kuti awapondereze; chifukwa cha iwo, Iye anadzudzula mafumu:


Mwana wamkazi wa Farao anapita ku mtsinje wa Nailo kukasamba ndipo adzakazi ake ankayenda mʼmbali mwa mtsinjewo. Tsono mwana wa Farao uja anaona kadenguko pakati pa mabango ndipo anatuma mdzakazi wake kuti akakatenge.


Kotero Mose ndi Aaroni anapita kwa Farao ndi kuchita monga momwe Yehova anawalamulira. Aaroni anaponya ndodo yake pansi patsogolo pa Farao ndi nduna zake ndipo inasanduka njoka.


Kenaka Yehova anati kwa Mose, “Farao ndi wowuma mtima. Akukana kulola anthu anga kuti apite.


Kenaka Yehova anati kwa Mose, “Mmawa, upite ukakumane ndi Farao maso ndi maso pamene azidzapita ku madzi ndipo ukanene kuti, ‘Yehova akuti, Lola anthu anga kuti apite akandipembedze.


Uyiwuze mfumuyo kuti, ‘Ine Ambuye Yehova ndikuti, “ ‘Ndine mdani wako, iwe Farao mfumu ya Igupto, iwe ngʼona yayikulu yogona pakati pa mitsinje yako. Umanena kuti, ‘Mtsinje wa Nailo ndi wanga; ndinadzipangira ndekha.’


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa