Ndipo ananenana wina ndi wina, Tiyeni tipange njerwa, tiziotchetse. Ndipo anali ndi njerwa naziyesa miyala, ndi katondo anayesa matope.
Eksodo 5:7 - Buku Lopatulika Musawapatsanso anthu udzu wakupanga nao njerwa monga kale; apite okha adzifunire udzu. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Musawapatsanso anthu udzu wakupanga nao njerwa monga kale; apite okha adzifunire udzu. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa “Musaŵapatsenso udzu wa njerwa anthu ameneŵa, monga muja munkachitiramu. Alekeni azikamweta okha udzuwo. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero “Inu musawapatsenso udzu wopangira njerwa monga mumachitira kale, iwo azipita ndi kukatenga udzu wawo. |
Ndipo ananenana wina ndi wina, Tiyeni tipange njerwa, tiziotchetse. Ndipo anali ndi njerwa naziyesa miyala, ndi katondo anayesa matope.
Ndipo muziwawerengera njerwa, monga momwe anapanga kale; musachepsapo, popeza achita ulesi; chifukwa chake alikufuula, ndi kuti, Timuke, timphere nsembe Mulungu wathu.
Ngakhale udzu ndi chakudya cha abulu athu ziliko; ndi mkate ndi vinyo zilikonso kwa ine ndi kwa mdzakazi wako ndi kwa mnyamata wokhala ndi akapolo ako; kosasowa kanthu.