nawawitsa moyo wao ndi ntchito yolimba, ya dothi ndi ya njerwa, ndi ntchito zonse za pabwalo, ntchito zao zonse zimene anawagwiritsa nzosautsa.
Eksodo 5:14 - Buku Lopatulika Ndipo anapanda akapitao a ana a Israele, amene ofulumiza a Farao adawaika, ndi kuti, Nanga dzulo ndi lero simunatsirize bwanji ntchito yanu yoneneka ya njerwa, monga kale? Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Ndipo anapanda akapitao a ana a Israele, amene ofulumiza a Farao adawaika, ndi kuti, Nanga dzulo ndi lero simunatsiriza bwanji ntchito yanu yoneneka ya njerwa, monga kale? Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Akuluakulu a thangata a Farao aja ankamenyanso akapitao Achiisraele amene adaŵaika kuti akhale omayang'anira ntchito, namaŵafunsa kuti, “Chifukwa chiyani lero simudaumbe chiŵerengero chonchija cha njerwa monga munkachitira kale?” Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Akapitawo a thangata a Farao ankawamenya oyangʼanira anzawo a Chiisraeli aja nawapanikiza kuti, “Chifukwa chiyani lero simunawumbe chiwerengero chovomerezeka cha njerwa monga chakale chija?” |
nawawitsa moyo wao ndi ntchito yolimba, ya dothi ndi ya njerwa, ndi ntchito zonse za pabwalo, ntchito zao zonse zimene anawagwiritsa nzosautsa.
Ndipo akufulumiza anawakakamiza, ndi kuti, Tsirizani ntchito zanu, ntchito ya tsiku pa tsiku lake, monga muja munali ndi udzu.
Pamenepo akapitao a ana a Israele anafika nalirira Farao, nati, Mwatero bwanji ndi akapolo anu?
Chifukwa chake atero Ambuye, Yehova wa makamu, Inu anthu anga okhala mu Ziyoni, musaope Asiriya; ngakhale amenya inu ndi chibonga, kapena kukusamulira iwe ndodo yake, monga amachitira Ejipito.