Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -




Eksodo 5:14 - Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

14 Akapitawo a thangata a Farao ankawamenya oyangʼanira anzawo a Chiisraeli aja nawapanikiza kuti, “Chifukwa chiyani lero simunawumbe chiwerengero chovomerezeka cha njerwa monga chakale chija?”

Onani mutuwo Koperani

Buku Lopatulika

14 Ndipo anapanda akapitao a ana a Israele, amene ofulumiza a Farao adawaika, ndi kuti, Nanga dzulo ndi lero simunatsirize bwanji ntchito yanu yoneneka ya njerwa, monga kale?

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

14 Ndipo anapanda akapitao a ana a Israele, amene ofulumiza a Farao adawaika, ndi kuti, Nanga dzulo ndi lero simunatsiriza bwanji ntchito yanu yoneneka ya njerwa, monga kale?

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

14 Akuluakulu a thangata a Farao aja ankamenyanso akapitao Achiisraele amene adaŵaika kuti akhale omayang'anira ntchito, namaŵafunsa kuti, “Chifukwa chiyani lero simudaumbe chiŵerengero chonchija cha njerwa monga munkachitira kale?”

Onani mutuwo Koperani




Eksodo 5:14
5 Mawu Ofanana  

Aigupto anachititsa moyo wa Aisraeli kukhala owawa kwambiri powagwiritsa ntchito yakalavulagaga yowumba njerwa ndi kuponda dothi lomangira, pamodzi ndi ntchito zina zosiyanasiyana zamʼminda. Iwo anakakamiza Aisraeli mwankhanza kuti agwire ntchito yowawayi.


Akapitawo a thangata aja anawafulumiza anthu aja nati, “Malizani kugwira ntchito yanu ya tsiku ndi tsiku monga mmene zinalili pamene munkapatsidwa udzu.”


Pamenepo oyangʼanira anzawo a Chiisraeli aja anapita kukadandaula kwa Farao kuti, “Chifukwa chiyani mwachitira antchito anu zotere?


Pa tsiku lomwelo Farao analamulira akapitawo a thangata ndi anzawo a Chiisraeli amene ankayangʼanira anthu kuti


Nʼchifukwa chake, Ambuye Yehova Wamphamvuzonse akunena kuti, “Inu anthu anga okhala mu Ziyoni, musawaope Asiriya, amene amakukanthani ndi ndodo nakumenyani ndi zibonga monga mmene Igupto anachitira.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa