Potero anawaikira akulu a misonkho kuti awasautse ndi akatundu ao. Ndipo anammangira Farao mizinda yosungiramo chuma, ndiyo Pitomu ndi Ramsesi.
Eksodo 5:10 - Buku Lopatulika Ndipo akufulumiza anthu ndi akapitao ao anatuluka, nanena ndi anthu ndi kuti, Atero Farao, Kulibe kukupatsani udzu. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Ndipo akufulumiza anthu ndi akapitao ao anatuluka, nanena ndi anthu ndi kuti, Atero Farao, Kulibe kukupatsani udzu. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Akuluakulu a thangata ndi akapitao Achiisraele adapita kukaŵauza anthu kuti, “Farao wanena kuti, ‘Sindidzakupatsaninso udzu. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Choncho akapitawo a thangata ndi anzawo a Chiisraeli amene ankayangʼanira anthu anapita kwa anthu aja nati, “ ‘Farao akuti sadzakupatsaninso udzu. |
Potero anawaikira akulu a misonkho kuti awasautse ndi akatundu ao. Ndipo anammangira Farao mizinda yosungiramo chuma, ndiyo Pitomu ndi Ramsesi.
Ndipo Yehova anati, Ndapenyetsetsa mazunzo a anthu anga ali mu Ejipito, ndamvanso kulira kwao chifukwa cha akuwafulumiza; pakuti ndidziwa zowawitsa zao;
Mukani inu nokha, dzifunireni udzu komwe muupeza; pakuti palibe kanthu kadzachepa pa ntchito yanu.
Katundu wa zilombo za kumwera. M'dziko lovuta ndi lopweteka, kumeneko kuchokera mkango waukazi, ndi wamphongo, mphiri, ndi njoka youluka yamoto, iwo anyamula chuma chao pamsana pa abulu, ndi ang'ono zolemera zao pa malinundu a ngamira, kunka kwa anthu amene sadzapindula nao.