Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -




Eksodo 5:10 - Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

10 Choncho akapitawo a thangata ndi anzawo a Chiisraeli amene ankayangʼanira anthu anapita kwa anthu aja nati, “ ‘Farao akuti sadzakupatsaninso udzu.

Onani mutuwo Koperani

Buku Lopatulika

10 Ndipo akufulumiza anthu ndi akapitao ao anatuluka, nanena ndi anthu ndi kuti, Atero Farao, Kulibe kukupatsani udzu.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

10 Ndipo akufulumiza anthu ndi akapitao ao anatuluka, nanena ndi anthu ndi kuti, Atero Farao, Kulibe kukupatsani udzu.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

10 Akuluakulu a thangata ndi akapitao Achiisraele adapita kukaŵauza anthu kuti, “Farao wanena kuti, ‘Sindidzakupatsaninso udzu.

Onani mutuwo Koperani




Eksodo 5:10
7 Mawu Ofanana  

Kotero anayika akapitawo kuti aziwazunza ndi kuwagwiritsa ntchito yolemetsa mokakamiza. Iwo anamangira Farao mizinda ya Pitomu ndi Ramesesi kumene ankasungirako chakudya.


Yehova anati, “Ine ndaona ndithu mazunzo a anthu anga amene ali ku Igupto. Ndamva kulira kwawo chifukwa cha anthu amene akuwapsinja, ndipo ndakhudzidwa ndi masautso awo.


Mʼmalo mwake mupite mukadzimwetere udzu kulikonse kumene mungawupeze. Komabe ntchito yanu sichepetsedwa.’ ”


Pa tsiku lomwelo Farao analamulira akapitawo a thangata ndi anzawo a Chiisraeli amene ankayangʼanira anthu kuti


Muwakhawulitse ndi ntchito anthu amenewa kuti azitanganidwa, asakhale ndi mpata omvera zabodza.”


Ngati wolamulira amvera zabodza, akuluakulu ake onse adzakhala oyipa.


Uthenga wonena za nyama za ku Negevi: Akazembe akuyenda mʼdziko lovuta ndi losautsa, mʼmene muli mikango yayimuna ndi yayikazi, mphiri ndi njoka zaululu. Iwo amasenzetsa abulu ndi ngamira chuma chawo, kupita nazo kwa mtundu wa anthu umene sungawathandize.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa