Ndipo anapanga mkhate wamkuwa, ndi tsinde lake lamkuwa, wa akalirole a akazi otumikira, akutumikira pa khomo la chihema chokomanako.
Eksodo 40:30 - Buku Lopatulika Ndipo anaika mkhate pakati pa chihema chokomanako, ndi guwa la nsembe; nathiramo madzi osamba. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Ndipo anaika mkhate pakati pa chihema chokomanako, ndi guwa la nsembe; nathiramo madzi osamba. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Kenaka adaika beseni losambira lija pakati pa chihema chamsonkano ndi guwa, nathiramo madzi osamba. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Iye anayika beseni pakati pa tenti ya msonkhano ndi guwa lansembe ndipo anathiramo madzi wosamba, |
Ndipo anapanga mkhate wamkuwa, ndi tsinde lake lamkuwa, wa akalirole a akazi otumikira, akutumikira pa khomo la chihema chokomanako.
Ndipo anaika guwa la nsembe yopsereza pa khomo la Kachisi wa chihema chokomanako, natenthapo nsembe yopsereza, ndi nsembe yaufa; monga Yehova adamuuza Mose.
Ukaikenso mkhate pakati pa chihema chokomanako, ndi guwa la nsembe, ndi kuthiramo madzi.
Ndipo ndidzakuwazani madzi oyera, ndipo mudzakhala oyera; ndidzakuyeretsani kukuchotserani zodetsa zanu zonse, ndi mafano anu nonse.
tiyandikire ndi mtima woona, m'chikhulupiriro chokwanira, ndi mitima yathu yowazidwa kuichotsera chikumbumtima choipa, ndi matupi athu osambitsidwa ndi madzi oyera;