ndipo Mose anautsa chihema, nakhazika makamwa ake, naimika matabwa ake, namangapo mitanda yake, nautsa mizati ndi nsanamira zake.
Eksodo 40:19 - Buku Lopatulika Ndipo anayalika hema pamwamba pa Kachisi, naika chophimba cha chihema pamwamba pake; monga Yehova adamuuza Mose. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Ndipo anayalika hema pamwamba pa Kachisi, naika chophimba cha chihema pamwamba pake; monga Yehova adamuuza Mose. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Pambuyo pake adautsa chihema pamwamba pa malo opatulikawo, nachiphimba ndi chophimbira chake cha chihema, monga momwe Chauta adamlamulira. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Kenaka anayika tenti pamwamba pa chihema ndipo anayika chophimba pa tenti monga momwe Yehova analamulira Mose. |
ndipo Mose anautsa chihema, nakhazika makamwa ake, naimika matabwa ake, namangapo mitanda yake, nautsa mizati ndi nsanamira zake.
Ndipo anatenga mboniyo, naiika m'likasa, napisa mphiko palikasa, naika chotetezerapo pamwamba pa likasa;
azinyamula nsalu zophimba za Kachisi, ndi chihema chokomanako, chophimba chake, ndi chophimba cha zikopa za akatumbu chili pamwamba pake, ndi nsalu yotsekera pa khomo la chihema chokomanako;