Eksodo 4:3 - Buku Lopatulika Ndipo ananena Iye, Iponye pansi. Naiponya pansi, ndipo inasanduka njoka; ndipo Mose anaithawa. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Ndipo ananena Iye, Iponye pansi. Naiponya pansi, ndipo inasanduka njoka; ndipo Mose anaithawa. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Chauta adamuuza kuti, “Taiponya pansi.” Mose ataiponya pansi ndodoyo, idasanduka njoka, iye nkuithaŵa njokayo. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Yehova anati, “Tayiponya pansi.” Mose anayiponya pansi ndipo inasanduka njoka ndipo anayithawa. |
Koma Yehova anati kwa Mose, Tambasula dzanja lako, nuigwire kumchira; ndipo anatambasula dzanja lake, naigwira, nikhalanso ndodo m'dzanja lake;
Pamene Farao adzalankhula nanu, ndi kuti, Dzichitireni chodabwitsa; pamenepo uzinena ndi Aroni, Tenga ndodo yako, iponye pansi pamaso pa Farao, isanduke chinjoka.
Kudzakhala monga munthu akathawa mkango, ndi chimbalangondo chikomana naye; kapena akalowa m'nyumba, natsamira kukhoma ndi dzanja lake, nimluma njoka.