Koma Zipora anatenga mpeni wamwala, nadula khungu la mwana wake, naliponya pa mapazi ake; nati, Pakuti iwe ndiwe mkwati wanga wamwazi. Ndipo Iye anamleka.
Eksodo 4:26 - Buku Lopatulika Pamenepo anati mkaziyo, Mkwati wamwazi iwe, chifukwa cha mdulidwe. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Pamenepo anati mkaziyo, Mkwati wamwazi iwe, chifukwa cha mdulidwe. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Choncho Chauta adamleka Mose osamupha. Ndiye pamene Zipora adanena kuti, “Ndiwe mkwati woomboledwa ndi magazi,” chifukwa cha kuumbalako. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Choncho Yehova anamuleka Mose wosamupha. Pa nthawiyo, Zipora anati, “Mkwati wa magazi,” ponena za mdulidwe. |
Koma Zipora anatenga mpeni wamwala, nadula khungu la mwana wake, naliponya pa mapazi ake; nati, Pakuti iwe ndiwe mkwati wanga wamwazi. Ndipo Iye anamleka.
Ndipo Yehova ananena ndi Aroni, Muka kuchipululu kukakomana ndi Mose. Ndipo anamuka, nakomana naye paphiri la Mulungu, nampsompsona.