Koma nsonga zake ziwiri za maunyolo opotawo uzimange ku zoikamo ziwiri, ndi kuziika pa zapamapewa ziwiri za efodi, m'tsogolo mwake.
Eksodo 39:4 - Buku Lopatulika Anapangira efodi zapamapewa zolumikizana; pansonga ziwirizo anamlumikiza. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Anapangira efodi zapamapewa zolumikizana; pa nsonga ziwirizo anamlumikiza. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Tsono adapanga tizikwewo tam'mapewa ta chovala cha efodi chija, tolumikizika ku chovalacho pa mbali zake ziŵiri. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Iwo anapanga efodi imene inali ndi timalamba tiwiri ta pa mapewa, tosokerera ku msonga zake ziwiri kuti azitha kumanga. |
Koma nsonga zake ziwiri za maunyolo opotawo uzimange ku zoikamo ziwiri, ndi kuziika pa zapamapewa ziwiri za efodi, m'tsogolo mwake.
Ndipo anasula golide waphanthiphanthi, nalemba nsambo, kuti amuombe pamodzi ndi lamadzi, ndi lofiirira, ndi lofiira, ndi bafuta wa thonje losansitsa, ntchito ya m'misiri.
Ndi mpango wa efodi wokhala pamenepo, wakummanga nao unali woombera kumodzi wa chiombedwe chomwechi; wa golide, ndi lamadzi, ndi lofiirira, ndi lofiira, ndi bafuta wa thonje losansitsa; monga Yehova adauza Mose.