Ndipo anapanga mitu iwiri ya mkuwa wosungunula, kuiika pamwamba pa nsanamirazo, msinkhu wake wa mutu wina unali mikono isanu, ndi msinkhu wa mutu unzake mikono isanu.
Eksodo 38:19 - Buku Lopatulika Ndi nsichi zake zinali zinai, ndi makamwa ake anai, amkuwa; zokowera zake zasiliva, ndi zokutira mitu yake ndi mitanda yake zasiliva. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Ndi nsichi zake zinali zinai, ndi makamwa ake anai, amkuwa; zokowera zake zasiliva, ndi zokutira mitu yake ndi mitanda yake zasiliva. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Nsaluzo adazikoloŵeka ku nsanamira zinai zokhala m'masinde anai amkuŵa. Ngoŵe za pa nsanamira, mitu yake ndi mitanda yake, zonsezo zinali zasiliva. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero pamodzi ndi mizati yake inayi ndi matsinde amkuwa anayi. Ngowe ndi zingwe zake zinali za siliva, ndipo pamwamba pake pa mzati anakutapo ndi siliva. |
Ndipo anapanga mitu iwiri ya mkuwa wosungunula, kuiika pamwamba pa nsanamirazo, msinkhu wake wa mutu wina unali mikono isanu, ndi msinkhu wa mutu unzake mikono isanu.
ndi nsichi zake makumi awiri, ndi makamwa ao makumi awiri akhale amkuwa; zokowera za nsichi ndi mitanda yake zikhale zasiliva.
Ndi nsalu yotsekera pa chipata cha pabwalo ndiyo ntchito ya wopikula, ya lamadzi, ndi lofiirira, ndi lofiira, ndi bafuta wa thonje losansitsa; utali wake mikono makumi awiri, ndi msinkhu wake ndi kupingasa kwake mikono isanu, yolingana ndi nsalu zotchingira za pabwalo.