Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -




1 Mafumu 7:16 - Buku Lopatulika

16 Ndipo anapanga mitu iwiri ya mkuwa wosungunula, kuiika pamwamba pa nsanamirazo, msinkhu wake wa mutu wina unali mikono isanu, ndi msinkhu wa mutu unzake mikono isanu.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

16 Ndipo anapanga mitu iwiri ya mkuwa wosungunula, kuiika pamwamba pa nsanamirazo, msinkhu wake wa mutu wina unali mikono isanu, ndi msinkhu wa mutu unzake mikono isanu.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

16 Adasungunula mkuŵa, napanganso mitu iŵiri, ndipo adaiika pamwamba pa nsanamira zija. Mutu wina kutalika kwake kunali mamita aŵiri nkanthu, ndipo winawo kutalika kwake kunalinso mamita aŵiri nkanthu.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

16 Anapanganso mitu iwiri ya mkuwa ndi kuyiika pamwamba pa nsanamira zija; mutu uliwonse unali wotalika kupitirirapo mamita awiri.

Onani mutuwo Koperani




1 Mafumu 7:16
8 Mawu Ofanana  

Popeza iyeyu anaunda nsanamira ziwiri zamkuwa, msinkhu wake wa imodzi unali mikono khumi mphambu isanu ndi itatu; ndipo chingwe cha mikono khumi mphambu iwiri chinayesa thupi la nsanamira imodzi.


Ndipo panali maukonde olukaluka ndi zoyangayanga, zokolana za pa mitu imene inali pamwamba pa nsanamira; zisanu ndi ziwiri za pamutu wina, ndi zisanu ndi ziwiri za pamutu unzake.


ndi nsanamira zake zisanu ndi zokowera zao; nakuta mitu yao ndi mitanda yao ndi golide; ndi makamwa ao asanu anali amkuwa.


Ndipo makamwa a nsichi anali amkuwa; zokowera za nsichi ndi mitanda yake zasiliva; ndi zokutira mitu yake zasiliva; ndi nsichi zonse za pabwalo zinagwirana pamodzi ndi siliva.


Ndi nsichi zake zinali zinai, ndi makamwa ake anai, amkuwa; zokowera zake zasiliva, ndi zokutira mitu yake ndi mitanda yake zasiliva.


Ndipo anapanga zokowera za mizati nsanamira ndi nsichi ndi masekeli aja chikwi chimodzi kudza mazana asanu ndi awiri mphambu asanu, nakuta mitu yake, nazigwirizanitsa pamodzi.


Ndipo korona wamkuwa anali pamwamba pake; utali wake wa korona mmodzi unali wa mikono isanu, ndi sefa ndi makangaza pakorona pozungulira pake, onse amkuwa: nsanamira inzake yomwe inali nazo zonga zomwezi, ndi makangaza.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa